Chakwera alangiza ophunzira pa sukulu ya LUANAR kuti atsogolere ntchito zotukula Malawi

Kondanani Chilimunthaka

Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera walangiza ophunzira omwe amaliza maphunziro awo pa sukulu ya ukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (LUANAR) kuti atsogolere ntchito yotukula dziko lino pa ulimi ndi chuma.

Polankhula lachinayi pa 21 Novembala 2024, pa mwambo wachisanu ndi chitatu opereka ma diploma ndi ma degree kwa omwe amaliza maphunziro awo a ukachenjede pa sukuluyi, Mtsogoleri wa dziko linoyu anati ndiwokondwa kuti anakhala nawo pa mwambowu omwe panali ophunzira ena kuchokera mmaiko akunja omwe amaliza maphunziro awo pa sukuluyi ndipo kuti ali ndi chikhulupiliro kuti ukadaulo omwe awupeza akagwiritsa ntchito potukula ntchito za ulimi ndi chuma.

Mtsogoleri wa dziko linoyu anati sukulu ya LUANAR yakhala sukulu yapamwamba yomwe yatulutsa akadaulo a maluso osiyanasiyana pa nkhani za ulimi.

“Chinthu chimodzi chomwe chimakonda ndi chakuti sukulu ino ndiyodzipereka kudzutsa maluso atsopano, ukadaulo komanso chidziwitso munduna wa malimidwe mosasiya gawo lina lililonse.

Utsogoleri wa sukulu ino udamvetsetsa kuti ngati tikufuna kukwanilitsa masomphenya okhala odzidalira pachuma pomanga maziko pa ukatswiri wa malimidwe a makono, tikuyenera kukhazikitsa njira zamakono zomwe mzothekera kuchita monga ife tifunira, komanso kukhalanawo akatswiri omwe ali ndi ukadaulo ogwiritsa ntchito njirazo moyenera” Anatero Mtsogoleri wa dziko lino yemwenso ndi Chancellor wa sukuluyi.

Iye anati kusintha kwa nyengo kwasokoneza zinthu zambiri mdziko muno, ndipo kuti zikusowekera ukadaulo omwe ophunzirawa awupeza pa nthawi ya maphunziro awo pa sukulu ya LUANAR.

Apa a Chakwera anati sukulu ya LUANAR ikutsogolera kusintha kwa kaganizidwe komwe dziko lino likufuna kuti likwanilitse masomphenya a mchaka cha 2063.

Mwa ophunzira 2,166 omwe amaliza maphunziro awo pa sukulu ya LUANAR, 689 ndi omwe analandira ma diploma ndi ma degree awo lachinayi, ndipo Mtsogoleri wa dziko lino anapereka K200,000 kwa ophunzira asanu ndi atatu (8) omwe achita bwino kwambiri kuposa anzawo pa maphunziro awo ngati njira imodzi yowayamikira komanso kulimbikitsa ena.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *