Mtsogoleri wa bungwe loona za ndale mdziko muno a Joseph Chunga apempha a Polisi mdziko muno kuti amange mukulu wa achinyamata mdziko muno a Paulos Norman Chisale kamba ka mau omwe cholinga chake kunali kukolezera ziwawa zinthu zomwe zili ndi kuthekera koyambitsa nkhondo mdziko muno.

Joseph Chunga

A Chunga adati palibe munthu yemwe ali pamwamba pa Lamulo kuphatikizapo a yemwe adali mtsogoleri wakale a Peter Mutharika.

Iwo ati zikuoneka kuti ngakhale DPP italowa mboma palibe chomwe chizasinthe kamba koti ikhoza kuzakhala yoipa kuposa kale.

Iwo adati a Malawi adachotsa DPP kamba ka mwano ndi zipongwe zomenya anthu. Koma apapa zikuoneka kuti DPP sidasinthe.

Nayatswiri andale mdziko muno adzudzula Mkulu wa achinyamata a Norman Paulos Chisale kamba ka uthenga wawo owoopseza komanso onyoza atsogoleri mdziko muno.

Dr Ben Dzolowere Komanso achinyamata ambiri adzudzula a Chisale kamba ka uthenga omwe uli ndi kuthekera kubweretsa ziwawa mdziko muno.

A Chunga adapereka chitsanzo kuti bungwe loona zakatangale limakwanitsa kutengera Wachiwiri kwamtsogoleri wadziko lino malemu Saulos Chilima kumabwalo azamilandu palibe cholakwika kukafusa mafunso a Mutharika.

Naye katswiri wina pa nkhani za ndale Dr Ben Dzolowere wadzudzula achisale kamba ka mau achipongwe.

“Munthawi ngati iyi pomwe tikuyandikira masankho, ndipoyenera kuti atsogoleri aziyankhula mfundo zokha zokha osati zinthu zomwe zingabweretse ziwawa,”Adatero a Dzolowere.

Nawo a Ceasar Kondowe ati zomwe apanga a Chisale ku Bangwe ndi nzomvetsa chisoni.

A Kondowe ati nthawi ngati iyi imafunika kuyankhula zomwe zipani zizapange zikawina.

Naye mkhala kale pa ndale a Unandi Banda adzudzula zomwe ayankhula a Chisale ponena kuti munthawi ya masankho izi zili ndi kuthekera kusokoneza masankho.

A Unandi adati Malawi ndi dziko la mtendere choncho a Chisale apewe kuyankhula zinthu zomwe zingabweretse nkhondo.

Iwo ngati ali ndi madando ali ndi ufulu kukadandaula ku mabungwe mongwe Human Rights Commission, Malawi Electoral Commission, komanso ku Police kumene.

Naye mkulu wakale wabungwe la Centre For Human and Rehabilitation a Undule Mwakasungula adzudzula chipani cha DPP ndinso a Norman Chisale kamba ka uthenga wawo ku Bangwe.

A Undule ati Malawi ndi dziko la bata ndinso mtendere.

MBIRI YA DPP

Kwa amene ayiwala kale, chipani cha DPP chimadziwika bwino ndi ziwawa. Chipani cha DPP chimadziwika ndi kumenya anthu mopanda chisoni or kupha kumene. Wanena izi ndi Shadreck Khan yemwe amapanga malonda ku bwalo la njobvu.
A Khan ati palibe zachilondo pa zomwe ayankhula a Chisale chifukwa izi ndi zomwe chimadziwa chipani cha DPP.

5 thoughts on “Akatswiri pandale apempha boma kuti limange a Paulos Norman Chisale kamba ka mau okolezera ziwawa”
  1. Ndizoona a Norman Chisale akuwoneka kuti alipamwamba pa lamulo ndiye akuyenela kumangidwa chifukwa mau omwe alankhula ndiwobweletsa chisokonezo mmdziko ananena kuti amemeza a chinyamata Njanje to Chitipa mau omwe Ali obweletsa mantha ku dziko komanso anati yemwe apite ku pegi house khomo lolowela akaliwona koma lotulukila sakalowona,ndipo ine ngati mmodzi mwa asilikali opuma iyeyu akuwononga mbiri ya asilikali opuma mdziko muno ngakhale Ali ndi ufulu olankhula.Akuyenela kumangidwa.Kunena kwa ndithe ndithe Nanthambwe anadzitemgela.

  2. Chisaletu is a toothless dog who can’t even bite… He has no any clue as to what it means to win back the government seat… That’s why he is busy inciting violence and castigating plus pushing the dpp cadets into violence… The law is yet to take it’s course on him

  3. DPP will never change, kuotcha anthu ku 24 banja la a Tambala lonse, komaso Chisale always ma speech ake amakhala ma nosense and obweretsa nkhondo pakati pa a Malawi, mtsogoleri ndi emweyu Dr LMC sakuchokaaa ❤️

  4. Boma likulakwisa kwambiri likulekelera munthu kumatha matha, kumatukwana ngati ali kunyumba kwake, kulitenga dziko ngati mkadzi wake.

  5. Uyuyu sikaswiri weniweni. Akanakhala kaswiri weniweni akanayamba kutuluka pazikwanje. Bwenzi onse azikwanje atatsekeredwa. Awa ndi aganyu a chipani.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *