Olemba : Alfred Chauwa 

A Malawi ochuluka omwe amayenda pa ma galimoto ati ndi okondwa kamba ka ganizo laboma lotsekulira gawo lina la msewu ochokera pa Hotela yotchuka ya Cross Roads mpaka ku Kanengo.

Izi akuti zikupangitsa magalimoto kuyenda mofulumira kuposa kale.

“Tiyamikile utsogoleri wadziko lino kamba kotsekula gawo limodzi la mseu wa Kanengo pano tikuyenda mosataya nthawi,” watero dalaivala Chimwemwe Yakobe yemwe amakonda kuyenda mu msewu umenewu.

Ndipo titayendera nseu umenewu tinaona anthu ambiri akukondwa ndi ntchito imeneyi.

Izi zikudza kamba ka ganizo la boma kudzera kwa a Jacob Hara omwe anatsekula gawo limodzi la ntchitoyo.

Izi zikutanthaunza kuti Omanga mseu umenewu pano azimanga gawo linalo lomwe ndi lomaliza pa ntchito yomanga nsewu ochokera pa Cross Roads kupita ku Kanengo.

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera adakhazikitsa ntchito yomanga nsewu umenewu kumayambiriro a chaka chino ku mwambo omwe udachitikila ku Dowa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *