Phungu wachinyamata Baba Malondera

Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera akupitilirabe kuchita dzchibwino kwa a Malawi.

Chakwera lero wayamba ntchito yogawa chimanga kudela la mfumu yaikulu Kalumbu kudzera ku nthambi yake ya boma yoona za ngozi zodza mwadzidzi la Dodma.

Mmawu ake phungu wa delaro a Baba Malondela ayamika a Chakwera kamba ka izi.

Iwo ati thandizo logawa chimanga ladza panthawi yake pomwe anthu mdela lake akubvutika ndi njala.

Mabanja 3,500 azilandila chimanga thumba limodzi kwa minyezi inayi.

Boma kudzela ku Dodma lidalengeza kuti ligawa chimanga ku mabanja okwanila 4 Million omwe akuvutika mmaboma onse amdziko muno.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *