Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera wafika mdziko muno lero pomwe iye adakakhala nawo pamsonkhano waukulu wa World Bank’s International Development Association (IDA) mdziko la Kenya. Chakwera adanyamuka pa ulendo umenewu dzulo kudzera pa bwalo lalikulu la ndege la Kamuzu International Airport (KIA). President Dr Lazarus McCarthy Chakwera being welcomed by his vice Dr Saulos Klaus Chilima Mukulankhula kwawo pa bwalo la ndege a Chakwera ayamikila bungwe la World Bank kamba koonetsa chidwi chotukula dziko lino. Chakwera adati bungwe la World Bank lakangalika ndipo laonetsa kudzipereka kofuna kutukula dziko la Malawi. Chakwera adalandilidwa ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino a Saulos Klaus Chilima, nduna za boma , atsogoleri achipani, akuluakulu aboma komanso otsatira chipani cha Malawi Congress (MCP). Post navigation Chakwera describes IDA as instrumental in Malawi’s recovery strategy President Chakwera appointed IDA SADC Champion