A Chakwera ayamikira mpingo wa CCAP Kondanani Chilimunthaka Mtsogoleri wa dziko la Malawi, Dr. Lazarus Chakwera wayamikira mpingo wa CCAP pogwira ntchito ndi boma mu zaka 100 zomwe wakhala okhazikika mdziko muno komanso maiko ena. Mmawu ake lamulungu pa Ogasiti 25, pomwe anakhala nawo pa mwambo okumbukira kuti padutsa zaka 100 chikhazikitsire mpingo wa CCAP omwe unachitikira pa bwalo la zamasewero la Civo mu mzinda wa Lilongwe, Pulezidenti Chakwera anati mpingo wa CCAP ndi anthu achuluka mmaiko osiyanasiyana monga Malawi, Zambia, Zimbabwe, komanso Mozambique. A Chakwera adati mu zaka zonsezi mpingo wa CCAP wakhala ukulimbikira kumutumikira Mulungu mmadera anayi monga ulaliki, kutumikira miyoyo ya anthu, kulimbikitsa kayendetsedwe kaboma kabwino, komanso kulimbikitsa kupemphera. “Mukati muyang’ane za maphunziro makamaka kwathu kuno, masukulu amene ndi a CCAP mngankhaninkhani, mukati muyang’ane ku nkhani ya umoyo, mupeza kuti zipatala zomwe zamangidwa ndi CCAP mdziko muno mzankhaninkhani, mukati muyang’ane zomangamangazi mupeza kuti manyumba a chipembedzo omwe amangidwa ndi CCAP mdziko muno mngankhaninkhani” Anatero Mtsogoleri wa dziko la Malawi. A Chakwera antiso mpingo wa CCAP wathandizira kumbali ya ulimi, kutukula chuma kudutsa mu ma bizimisi osiyanasiyana. “Lero tikungoyenera kukuthokozani komanso kukulimbikitsani kuti musasiye kugwirana manja ndi a Malawi komanso ndi boma pa ntchito ya chitukuko” anawonjezera motero Pulezidenti Chakwera. Pakadali pano Pulezidenti Lazarus Chakwera wapempha a Malawi kuti akhale oyanjana kuti boma liziyenda bwino ndipo kuti chitukuko chipitilire kukwera mdziko muno. Mpingo wa CCAP pakadali pano uli ndi ma Sinodi asanu omwe ndi Livingstonia, Nkhoma, ndi Blantyre kuno ku Malawi, komanso Zambia mdziko la Zambia, ndi Harare mdziko la Zimbabwe. Post navigation Ngora boss Chileka Banda hits back at accusations of taking part in politics while a public servant: “I have not flouted any law.” Judicial Complex in Lilongwe takes off with a bang