Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus McCarthy Chakwera akupitiliza ntchito yogawa chimanga kwa a Malawi omwe akukhudzidwa ndi njala.

Izi zikugwirizana ndi mawu omwe a Chakwera adanena m’nyumba ya Malamulo kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe atafe ndi Njala mdziko muno.

Tikunena pano, Boma kudzera ku nthambi yoona za Ngozi zogwa mwadzidzidzi ku Mangochi yagawa kale chimanga ku mabanja wokwana 50,642 , pamene nthambi yomweyi yagawa chimanga m’boma la Neno ku mabanja okwana 6,000.

Polankhula m’boma la Lilongwe kwa Mfumu Chiwaula , Mlembi wamkulu ku nthawi yoona za ngozi a Charles Kalemba ati anthu okwana 4 Million ndi omwe akuyembekezeka kulandila chimanga chaka chino kufikila kumaymbirilo a chaka cha mawa.

A Kalemba adati ntchito yogawa chimanga inayamba nsanga chaka chino kamba ka mabvuto a zachilengedwe monga ng’amba komanso Tropical Cyclone Freddy.

Kupatula Mangochi, Lilongwe ndi Neno, Boma lafikila maboma ena monga Nsanje ndi wena otere.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *