Mkulu wa Banki yaikulu ya m’dzimo muno ya Reserve Dr Wilson Banda watsutsa phekesera zomwe zikumveka maka pa masamba a michezo zomwe a Malawi ambiri akugawana kuti Boma lili ndi malingaliro opanga ndalama yogwirana yokwana K10,000. Poyankhapo pa nkhaniyi , a Banda anati boma lilibe maganizo opanga ndalama yamtundu umenewu. Iwo anati pamakhala ndondomeko zomwe Bankiyi imayenera kutsatira kuti izi zitero ndipo imodzi mwa ndondomeko imeneyo ndiyo kuti pakuyenera kukhala kufunika kuti izi zitero zomwe pakadali pano palibe. Mwa ichi, a Banda apempha olemba nkhani komanso ogwiritsa ntchito ma tsamba a michezo monga ma WhatsApp ndi ma Facebook kuti apewe kufalitsa nkhani zomwe zilibe umboni chifukwa zimenezo zili ndi kuthekela koononga chuma cha dziko lino. A Banda ati ma ofesi awo ndi otsekula ndipo atha kumafusa aliyese maka mneneli wa Bankiyi komanso azitsogoleri wena ndi wena ku Bankiyi. Post navigation Castel Malawi brings Spirits of Malawi festive editions NBM concludes ’12 Days of Christmas’ initiative