A Malawi awalangiza kuti ayike chidwi chawo pa nkhani ya ulimi othilira pogwirita ntchito zipangizo za luso loyendela mphepo.

Mkulu wa Kampani ya Africa Windmill a Gibozi Mphanzi ndi amene anena izi m’mzinda wa Lilongwe.

A Mphanzi ati anthu amene anawaikila zinthu anga izi akhala akupeza phindu kuchokera mu ulimi odalira zipangizo zoyendera mphepo. A Mphanzi ati alimi ambiri apeza ndalama monga ma K1 Million wena ma K800,000.

Pakadali pano a Mphanzi apempha a Malawi kuti ayambe kugwiritsa ntchito zipangizo izi chifukwa sizikhala ndi zambiri zolowetsa.

 

Kampani ya Windmill Africa ipempha a Malawi kuti ayambe kugwiritsa ntchito zipangizo zoyendera mphepo

 

 

 

 

 

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *