Apereka ndondomeko ya ma ufulu ku Dakar Senegal Malawi ndi dziko limodzi lomwe mbiri yake ili bwino kwambiri pankhani dzokhuza ma ufulu osiya na siyana. Izi zadza kamba koti mtsogoleri wadziko lino waikapo chidwi kwambiri kuonetsetsa kuti Malawi achite bwino. Posachedwapa Malawi inakhala nawo pansonkhano waukulu ku Dakar m’dziko la Senegal komwe maiko anakambirana mozama nkhani za ma ufulu. Mmodzi mwa ogwira ntchito ku Ethiopia kuimila Malawi kumeneko Luke Tembo ndi amene anaimilira mtsogoleri wa dziko la Malawi. A Tembo adapereka masomphenya omwe Malawi alinayo pofuna kupititsa ntchito ya ma ufulu mdziko muno. A Tembo adaperekaso report ya mmene Malawi ikuchitira pankhani ya ntchito yopititsa patsogolo ma ufulu awanthu. Ndipo pomaliza maiko ochuluka anayamikila Malawi kamba kopititsa patsogolo ma ufulu osiyasiyana. Zomwe likupanga boma la a Chakwera zikusiyana ndi zomwe limapanga boma la a Peter Mutharika lomwe silimapereka ma report anga awa ku mabungwe owona za ma ufulu (The African Commission on Human and Peoples’ Rights and the African Union Permanent Representatives Committee Sub-Committee on Human Rights, Democracy and Governance). Post navigation Chipasupasu chabuka mchipani cha DPP pa nkhani ya oyenela kuponya vote ku msonkhano wa ukulu wa convention Nduna Richard Chimwendo Banda ipempha Mafumu kuti athandize Chakwera pa nkhondo yolimbana ndi katangale