Mkhalakale pa nkhani yoona ntchito za ulamuliro wabwino a Raymond Likambale ayamikila ntchito yogawa chimanga yomwe boma la Lazarus McCarthy Chakwera likupanga mmaboma onse okhudzidwa ndi njala.

A Likambale ayankhula izi mumzinda wa Lilongwe patapita nthawi pang’ono boma kudzera ku bungwe loona za Ngozi zogwa mwadzidzidzi litalengeza kuti lili ndi malingaliro ogawa chimanga ku mabanja 4 million.

A Likambale ati ntchito yogawa chimanga ithandiza kwambiri nzika zomwe zambiri mwa izo zili pa vuto la njala.

A Likambale apemphaso boma kuti ntchitoyi ifikire anthu ambiri osati monga alengezera kuti 4 million yokha.

“Ambiri ali pa chiopsezo cha njala choncho boma lifikire anthu onsewo, ”adatero a Likambale.

Ntchito yogawa chimanga kwa anthu 4 million ikugwirizana ndi mawu omwe Chakwera adanena mnyumba ya Malamulo kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe atafe ndi Njala mdziko muno.

Tikunena pano, Boma kudzera ku nthambi yoona za Ngozi zogwa mwadzidzidzi ku Mangochi yagawa kale chimanga ku mabanja wokwana 50, 642 , pamene nthambi yomweyi yagawa chimanga m’boma la Neno ku mabanja okwana 6,000.

Kwina komwe apereka chimanga ndi ku Nsanje, Chiladzulu, Mzimba, Lilongwe, Zomba , Machinga, Mulanje, Blantyre, Phalombe, Mwanza, Ntcheu and Nkhotakota.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *