Mfumu yayikulu Kawinga ya a Yao, mdziko muno, yati ndi yokondwa kuti m’sukulu zosiyanasiyana m’dziko muno kuphatikizapo za m’boma la Machinga mukuchitika zitukuko zomwe cholinga chake ndi kutukula maphunziro. Mfumuyi yanena izi ku Machinga pomwe nduna ya zamaphunziro a Madalitso Kambauwa Wirima amayendera ntchito yomanga midadada itatu ya zipinda zophunziriramo pa sukulu ya pulayimale ya Kanjedza m’bomali. M’mawu ake a Kambauwa Wirima anati motsogozedwa ndi masomphenya a mtsogoleri wadziko lino Dr. Lazarus McCarthy Chakwera, unduna wawo ukumanga zipinda zatsopano zophunziriramo zokwana 10900 komanso zipinda zosinthiramo atsikana zokwana 1000 m’sukulu zosiyanasiyana m’dziko muno pansi pa ndondomeko yotchedwa Malawi Education Reform Programme (MERP). Hon Minister Kambauwa Wirima “Kudzera mu ndondomekoyi boma likuperekanso ndalama zomwe sukulu zikugwritsa ntchito, tikuzamitsanso luso la utsogoleri kwa adindo a pasukulu, kulemba ntchito atsikana olimbikitsa atsikana anzawo maphunziro zomwe cholinga chake ndi kutukula maphunziro mogwirizana ndi zomwe zili mu masomphenya a Malawi 2063,” anatsiriza motero a Wirima. Atachoka pa sukulu ya Kanjedza, a Wirima anakayenderanso ntchito ngati yomweyi pa sukulu ya pulayimale ya Ferry m’boma la Balaka komwe anaonetsa kukondwa kwawo ndi m’mene ntchitoyi ikuyendera. A Ibrahim Chipojola omwe ndi wapampando wa komiti yoyendetsa ntchito zachitukuko anati ndi wodzipereka kuthandizana ndi boma potukula maphunziro pasukuluyi. Iwo anapitiriza kuyamikira boma poganiza zoonjezera zipinda zophunziriramo pasukuluyi pomwe akuti pali ophunzira ochuluka. Malinga ndi a Wirima ntchito yomanga midadadayi ikadzatha idzathandiza kuchepetsa chiwerengero cha ophunzira omwe mphunzitsi m’modzi amakhala nawo mkalasi. Pofunanso kupititsa patsogolo maphunziro a luso lamakono, boma lagawa kale matabuleti m’sukulu za pulayimale zoposera 490 m’zigawo zonse zisanu ndi imodzi zamaphunziro, pansi pa ndondomeko ya Building Education Foundation through Innovation and Technology (BEFIT). Ndomekoyi ikulunjika chaka cha 2029 pomwe ana onse ophunzira m’sukulu zapulayimale adzakhale akugwiritsa ntchito matabuleti am’manja pophunzira. Post navigation Arkridge pays examination fees for all Zomba Malosa needy students Curricula review crucial – Minister Wirima