Chakwera wapititsa patsogolo ntchito ya za Umoyo Zukhala ngati nkhambakamwa koma ayi ndithu izi zeni zeni. Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera lero watsindikanso kuti wayika chidwi chachikulu pogwira ntchito za umoyo mdziko muno. Izi wayankhula lero pomwe iye amapereka mfundo zikulu za momwe nkhani ya chuma ikuyendera mdziko muno. Mu ndondomeko ya ndalama ya mchaka cha 2023 mpaka 2024 Dr Lazarus chakwera wakwanilitsa kupanga zinthu zambiri zolozeka komanso zapamwamba. Boma la Dr Lazarus chakwera mogwilizana ndi unduna wa za umoyo wakwanitsa kupeleka katemera wa matenda monga a Covid 19 ,Polio komaso cholera. Dr Lazarus chakwera wakwanilitsa kubwezeletsa chikhulupiliro cha anthu ndi mabugwe akunja omwe amathandiza ntchito za umoyo mdziko muno mchifukwa chake posachedwapa unduna wa za umoyo walandira ndalama zokwana $517 Million yomwe ithandize kulimbana ndi matenda a Aids, Tb komaso Malungo. Mtsogoleri wa dziko lino akumanga chipatala cha khansa chomwe chikuyembekezeka kuyamba kuthandiza anthu omwe apezeka ndi matenda akhasa mdziko mwathu momuno. Unduna wa za umoyo wakwanilitsa kulemba ntchito achinyamata okwana 3, 930 ongogwira ntchito moyembekezera komaso uli ndi chikozero cholembaso ntchito anthu okwana 2, 741 okhazikika omwe agwire ntchito yothandiza ku undunawu. Dr Lazarus chakwera wakwanilitsa kumanga zipatala 200 zazing’ono za madera zomwe zikuthandiza kuchepetsa kudzadzana kwa odwala mzipatala zikuluzikulu za mdziko muno. Post navigation Authorities commends Malawi Red Cross Society for supporting measles campaign Enact Termination of Pregnancy Bill to save women’s lives, – CSOs