Bungwe la United Nations (UN) layamikila mtsogogoleri wadziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera kamba koonetsa chidwi pa ntchito yotukula amai mdziko muno.

Rebecca Adda-Dontoh walankhula izi dzulo pame mtsogoleri wadziko lino anakumana anthu ogwira ntchito kumabungwe a UN.

M’mawu awo a Dontoh anayamikila a Chakwera kuti amai akusimba lokoma mdziko muno chifukwa chakwera akuwapatsa mpata otsogolera nawo mzochitika chitika za dziko.

A Dontoh anayamikilaso a Chakwera kamba ka ma ufulu wachibadidwe omwe a Malawi akusangalala nawo.

“Ngakhale UN ndi yokondwa komanso maiko ambiri akukondwa ndimmene nkhani za ma ufulu zikuyendera mdziko muno,” adatero a Dontoh.

Mmawu ake Mtsogoleri adziko lino adayamikila ma bungwe a UN kamba ka thandizo lomwe akupereka kudziko lino la Malawi.

Iwo anapereka chitsanzo cha mmene UN idathamangira pa nthawi ya ngozi ya Namondwe omwe anachitika chaka chatha.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *