Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera watsimikizira anthu ochita malonda mdziko muno kuti Boma lipanga chilichonse chotheka pofuna kupititsa patsogolo miyoyo ya anthu ochita malonda mdziko muno. A Chakwera anena izi pam’kumano omwe unachitika ku nyumba ya chifumu ya Kamuzu Palace pamene iwo amayankhula ku ma venda okwana 800 ku Kamuzu Palace mumzinda wa Lilongwe. Dr Lazarus McCarthy Chakwera A Chakwera anadzudzula magulu wena a wanthu amene amaonongera dala zinthu ndi cholinga choti zikaonongeka azipeza zoyankhula. A Chakwera adandaula ndi mchitidwe ofuna chikole ndi cholinga choti munthu alandire ngongole kamba kakuti a Malawi alibe chikolecho. Chakwera walonjeza kuti akhala pansi ndi amabungwe okongoza ndalama la NEEF komanso mabungwe wena obwereketsa ngongole kuti awone zomwe angachite. Chakwera watsindika kuti ma venda ndi anthu ofunika kwambiri pa chitukuko chadziko lino. Mtsogoleriyu adalangizanso bungwe la Malawi Revenue Authority (MRA) kuti asamatchaje chimtengo chachikulu cha misonkho. Post navigation 90% recovery to resume operations at immigration Vendors describe Chakwera leadership as unique