Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera lachinayi anapita kukayendera kukacheza ndi omwe adakhudzidwa ndi bvuto losefukila kwa madzi mboma lija la Nkhota Kota.

Poyankhula mmau ake atatha kuyendera anthu , Chakwera analimbikitsa onse okhudzidwa kuti boma lionetsetsa kuti aliyese wathandizika ndipo wayambaso moyo watsopano.

Dr Lazarus McCarthy Chakwera

Chakwera adatsimikizira anthu okhudzidwawo kuti boma lake lipanga zosetha kuti zinthu zikhale mchimake.

Pamwambowo, Chakwera anatsindika kufunika kuti anthu mdziko muno ayambe kumanga zinthu zomwe zingalimbe nthawi ya ngozi monga yosefukira kwa madzi.

Chakwera adapemphaso akufuna kwabwino kuti athandize anthu omwe akunzunzika kamba kosefukila kwa madzi.

Pomaliza Dr Lazarus chakwera wapemphaso nzika za dziko lino kuti zipewe kumanga nyumba malo omwe ali ndi chiopsezo chakuti tsiku lina madzi akhoza kudzafikako.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *