Mabungwe omwe si aboma otchedwa Independent Civil Society (ICSO) adzudzula mabungwe anzawo omwe si aboma kamba kamba komapereka mpungwe pungwe kwa mtsogoleri wa dziko lino mdzina lomenyera ma ufulu.

Mabungwe omenyera ufulu wa a Malawi

Mabungwe we pompano adapereka madiku asanu ndi awiri (7) kwa mtsogoleri wa dziko lino kuti atulutse lipoti lomwe adatulutsa bungwe lapadera lomwe mtsogoleri wadziko lino adasankha.

Koma mukulankhula kwawo pamsonkhano wa olemba nkhani, wapampando wa bungweli , Ceasar Kondowe, adati kupereka nthawi yokakamiza mtsogoleri wa dziko pa zinthu ndi kulakwa kwakukulu , kusowa mwambo komanso kudelera utsogoleri wa dziko.

Iwo adati a Chakwera asatulutse lipoti monga mabungwe wena akufunila chifukwa a Chakwera akugwiritsa kale ntchito lipotilo poyendetsela ntchito za boma.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *