Mtsogoleri wa Dziko lino a Lazarus Chakwera kudzera ku bungwe lija la Agricultural Commercialization Project (AGCOM) lero wapereka ndalama zokwana K6.5Billion ku mabungwe a zaulimi (ma cooperatives) okwana 63.

Ndalama izi zaperekedwa lero mboma la Mangochi pamwambo omwe unduna wa za ulimi unakonza mbomalo.

A Sam Kawale kupereka ndalama lero ku Mangochi

Mukulankhula kwawo m’malo mwa mtsogoleri wa dziko lino , nduna ya za ulimi a Sam Kawale anati ndi okondwa kuti zinthu zikutheka pansi pa utsogoleri wa Dr Lazarus Chakwera.

A Kawale adati “Ndine okondwa kuti lero, ndinali m’mudzi wa Mbinda, mmudzi mwa mfumu yaikulu Nankumba, Mangochi, kumene tapeleka ndalama zokwana K6,505,574,439.71 (K6.5 Billion) ku magulu okwana 63 mu program ya AGCOM, ”

Iwo adati , AGCOM ndi program imene ikupeleka ndalama ku magulu osiyana siyana m’dziko lonse kuti anthu azipanga business ya ulimi.

Gawo loyamba la Program ya AGCOM inali ndi ndalama pafupifupi K100 billion.

“Pano tili pa AGCOM 2 imene ili ndi ndalama zoposa K550 billion. Mukhoza kulembela ku bungweli kuti mupindule nawo. K6.5 billion imeneyi yapelekedwa ku magulu amene akwanilitsa kukhala ndi 30% ngati mbali yawo kuti alandile, ndipo aonetsa kuti apanga bizinesi ya phindu ndipo mabanja awo komanso dziko lipindula, ” Adatero a Kawale.

Malingan ndi a Kawale, magulu 63 amenewa akuchokela ku maboma oposa 15 mu Dziko lino la Malawi.

Mkulankhula kwawo, Mkulu wa AGCOM , Ted Nakhumwa wati cholinga cha AGCOM 2 ndi kuonetsetsa kuti alimi akupanga katundu wapamwamba.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *