Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera wati ndi okhumudwa kuti pali anthu wena amene sakugona tulo omwe amafuna kupeza njira zofuna kubela alimi afodya.

“Olo kuno kumudzi, ine, a Vice President Chilima, ndi nduna zonse timakhalira kusakasaka njira zoti tikuthandizeni alimi afodya kuti wina asakudyereni masuku pamutu. Komanso ndithokoze ma kampani amene mumagula fodya
wathu kuno ku Malawi kuti mwakhala mukutimvera kuti mitengo yogulira fodya izikhalanso yokomela mlimi,”

Lero lidali tsiku lalikulu m’mbiri ya boma la Kasungu pomwe Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Mccarthy Chakwera adagwira ntchito zosiyana siyana m’boma La kasungu malingana ndi chikalata watulutsa mlembi wamkulu wa boma mayi Colleen Zamba.

Chakwera adakayendera nyumba za asirikali a nkhondo zomwe boma la Malawi Congress (MCP) lamanga ku Engineering Battalion.

Komanso Chakwera adatseguliranso ofesi ya bungwe La Tobacco Commission lomwe lamangidwa m’boma la Kasungu.

Atachoka ku ku ofesi ya TC , m’boma La kasungu mtsogoleri wa dziko lino adakayendera fodya ku msika wa Chinkhoma.

Pomaliza pa zonse mtsogoleri wa dziko lino adatsegulira msika wa fodya pa sukulu ya vivya mdela la mfumu yayikulu Njombwa pomwe akulu aboma ndi abungwe la TC adayankhula.

 

 

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *