Bungwe la World Bank lalonjeza kuthandiza dziko la Malawi ndi ndalama zokwana $350Million kuti zithandize ntchito yomanga malo opukusira magetsi a Mpatamanga Hydropower Project.

Bank yaikuluyi yalengeza izi kupereka mudziko la America pamsonkhano wadzachuma wa World economic Summit (WES).

Izi zatheka kamba ka utsogoleri wabwino wa Dr Lazarus McCarthy Chakwera omwe akuimilidwa ndi nduna ya zachuma a Simplex Chithyola Banda.

Malo amenewa azipanga mphamvu za magetsi zokwama 361Megawatts.
Akatswiri ayamikira izi kuti zithandiza kutukula chuma cha dziko lino.

 

One thought on “Banki yaikulu padziko lonse lapansi World Bank ipereka ndalama zokwana $350Million ku boma la Malawi”

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *