Mkulu wa achinyamata mu m’chipani cha Malawi Congress a Richard Chimwendo Banda lero anapangitsa msonkhano wa mundipondera mwana pa bwalo la zamasewero la Dowa.

Mukulankhula kwawo a Chimwendo adati pakali pano palibe amene angatanganidwe kufuna kuvotera chipani cha Democratic Progressive (DPP) ndi mtsogoleri wake a Peter Mutharika chifukwa a Malawi anada nawo kukhosi.

Olemekezeka a Richard Chimwendo Banda

Iwo anati a Malawi akadakumbukira nkhanza zonse chomwe chipani cha DPP chimapanga.
Pachifukwachi, a Chimwendo anauza a Malawi kuti nthawi yakwana yoti monga dziko agwire ntchito ndi mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus McCarthy Chakwera.

Achimwendo adatchula zitukuko zikulu zikulu zomwe boma la Chakwera likupanga monga kumanga misewu posepose, midadada ya makalasi m’ masukulu okwana 11,000, kulemba adziphunzitsi ochuluka, anamwino, komanso kukweza pa udindo ogwira ntchito m’boma.

Mukulankhula kwawo nayo mfumu yaikulu Msakambewa , inayamikira Mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera kamba ka zitukuko migolo migolo.

Mfumuyi inapereka chitsanzo cha mmene wasinthira Lilongwe pakanthawi kochepa komwe Chakwera wakhala pa mpando ngakhale walowa pa udindo pa nthawi ya Covid – 19 ndinso milili
ina.

A Chimwendo sadali okha kumeko. Kunalinso nduna yoona kuti pasakhale kusiyana pakati pa amai ndi abambo a Jean Sendeza, Nduna yazaulimi a Sam Kawale, wachiwiri kwa Nduna ya za umoyo a Halima Daudi, Nduna ya malo a Deus Gumba.

Naye Wapampando wa chipanichi mchigawo cha pakati a Patrick Zebron Chilondola anali nawonso komweko.

 

 

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *