Mtsogoleri wa dziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera ayamikira mpingo wa African Methodist Episcopal kamba ka ntchito zabwino zomwe ukupanga mdziko muno.

A Chakwera ayankhula izi pamwambo omwe mpingowu umakumbukira kuti wakwanitsa zaka 100 uli mdziko muno.

Mukulankhula kwawo a Chakwera apempha a Malawi kuti azilemekeza anthu monga a Hannock Msokera chifukwa iwo anagwira ntchito yaikulu kuti dziko la Malawi lipeze mtendere.

A Chakwera anadandaula kuti Mdziko muno, tili ndi vuto loyiwala mbiri yathu ndikunyalanyaza komwe tachokela.

“Anthu ambiri saadziwa kuti African Methodist Episcopal Church ndi mpingo ofunikira mu mbiri ya dziko lathu. Koma zoona zake nzoti kupanda mpingo umenewu, tate wafuko lathu, malemu Angwazi Dr. Hastings Kamuzu Banda,
sanakapeza mwayi okaphunzira sukulu zapamwamba ku America, sukulu zomwe zinawaphunzitsa udokotala komanso kudana ndi mchitidwe wa chitsamunda,” Iwo adatero.

A Chakwera adati ichi mchifukwa chake zaka 50 zapitazo, mu chaka cha 1974, angwaziwo anafika ku Kasungu kuzapereka ulemu ku
mpingo ndi Abusa Hannock Msokera Phiri omwe unamupatsa kuthekera ndi upangili omwe anaugwiritsa ntchito pothana ndi boma lachitaganya.

Achakwera adayamikira mpingowo kamba kokonza mwambo umenewo.

“Ndiye lero ndi tsiku lopamba kwambiri kuti mpingo omwe unatichitira izi wasungidwa ndi Mulungu zaka 100, chomwe chiri chikumbutso kwa ife kuti Mulungu amasunga anthu ake komanso amasunga anthu amene amazipereka pa ntchito yomanga dziko. Sikuti nthawi
yomwe mpingowu umapanga zimenezi, mdziko muno,”

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *