Mkulu wa nthambi ya Malawi Defence Force (MDF) a Paul Valentino Phiri wapempha a Malawi kuti apewe kufalitsa nkhani za boma zokhudza ngozi ya ndege.

Mukulankhula kwawo mumzinda wa Lilongwe, a Phiri adati, ndikulakwa kumafalitsa ma uthenga abodza okhudza zinthu zomwe iwo alibe nazo umboni.

Iwo adapereka uthenga wa mbiri ya ndege yomwe idagwa omwe udaonetsa kuti ndege imeneyo adaiwona komaliza zija pa chingerezi amazi service , m’mwezi wa March 2024.

Ndipo imayembekezereka kupangidwanso service m’mwezi wa July 2024.

A Phiri adati nthambi yawo ya MDF yakonza dongosolo lapadera lomwe cholinga chake ndikuona chomwe chidachitika kuti ndege igwe.

Iwo adapempha a Malawi kuti adekhe ndipo zonse adzauzidwa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *