Mfumu yaikulu ya Maseko Ngoni Inkosi ya Makhosi Gomani 5 yapempha bata ndi mtendere mdziko muno pamene dziko la Malawi likupitilira kukhuza imfa ya yemwe adali wachiwiri kwa Mtsogoleri wadziko lino a Dr Saulos klaus Chilima. Pempholi ladza pamene achinyamata wena usiku wathawu akhala akugenda magalimoto osiyana siyana pamene amapita kuperekeza a Chilima. Mukulankhula kwawo ku Nsipe , Ntcheu pa mwambo operekeza a Chilima, a Gomani adati ndikofunika kwambiri kusunga bata chifukwa malemu Chilima adali munthu okonda mtendere. Mfumu yaikulu Gomani idati Maseko Ngoni yataya munthu ofunika kwambiri omwe udali mzati waukulu mboma la Ntcheu komanso dziko lonse la Malawi. Mfumu Gomani adati a Chilima adzawakumbukira ngati munthu munthu oopa Chauta komanso okonda banja lake. Post navigation UTM Regrets Provocative Remarks Amidst Turmoil Following the Death of Vice President Dr. Saulos Chilima President Chakwera leads thousands in bidding farewell with the Malawi Vice President Dr Saulos Klaus Chilima