Mgwirizano wa ma Bungwe omwe umamenyera ma ufulu osiyanasiyana mdziko muno la National Advocacy Platforms (NAP) layamikira mtsogoleri wa dziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera kamba kochita machawi posankha wapampando wa bungwe loona zamasankho la Malawi Electoral Commission (MEC).

Malingana ndi chikalata chomwe bungweli latulutsa chomwe wasainira ndi mkulu wabungweli a Benedicto Kondowe , anenetsa kuti izi zimalimbikitsa ulamuliro wabwino.

A Kondowe afunira mafuno abwino a Annabel Mtalimanja patchito yawo yomwe apatsidwayi komanso iwo afuniranso ma komishonala onse omwe asankhidwa.

A Kondowe ayamikira wapampando wakale a Chifundo Kachale kamba kogwira ntchito yawo modzipereka ndinso motsata malamulo.

Malingana ndi chikalata chomwe bungwe Malawi Electoral Commission (MEC) latulutsa, a Chakwera asankhaso abusa a Phillip Kambulire kukhala komishonala wa bungweli malingana ndi gawo 75 la malamulo adziko lino.

Ena omwe asankhidwa ndi a Dr. Limbikani Kamlongera , Richard Chapweteka ,
Dr Emmanuel Fabiano, Francis Lazalo Kasaila ndi Caroline Mfune.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *