Zikalata za ofuna kupikisana ku nsonkhano wawukulu wa MCP ziyamba kupezeka lolemba

Kondanani Chilimunthaka

Chipani cholamula cha Malawi Congress chawuza mtundu wa a Malawi kuti mafomu omwe amene akufuna kukapikisana nawo mmaudindo osiyanasiyana kunsonkhano wake wawukulu omwe ukuyembekezeka kuchitika kuyambira pa Ogasiti 8 mpaka pa Ogasiti 10 ziyamba kupezeka lolemba likudzali pa Julayi 1 kulikulu la chipanichi komanso mmaofesi onse a mzigawo.

Watsimikiza izi ndi mkhala pampando wa nsonkhano wawukulu wa chaka chino mchipani cha MCP, a Kezzie Msukwa omwenso ndi mkhala pampando wa chipanichi mchigawo cha Kumpoto-Kumpoto (NN) pa nsonkhano omwe anachititsa ndi akuluakulu ena a chipani cha MCP kulikulu lake mu mzinda wa Lilongwe.

Polankhula loweluka mmawa pa Julayi 29, 2024 pomwe amadziwitsa a Malawi mulingo omwe zokonzekera za chisankhochi zafika, a Msukwa anati zokonzekera zambiri zatha ndipo kuti tsopano mafomu omwe okapikisana akuyenera kutenga ayamba kupezeka lolemba likudzali.

Koma mwa zina a Msukwa omwe anatsagana ndi Nduna yowona zofalitsa nkhani yemwenso ndi Mneneli wa boma a Moses Kunkuyu, omwe akutsogolera gawo la madongosolo a nsonkhanowu, komanso a Joseph Njobvuyalema omwe akutsogolera kawuniwuni wa oyenera kuyima, atsindika kuti kunsonkhanowu okhawo omwe akhalapo mmaudindo osiyanasiyana mchipanichi kwa zaka ziwiri kuchokera ku ma eliyo, maboma kukafikira ku likulu la chipani (NEC) ndi omwe ali oyenera kukapikisana nawo ku nsonkhano osankha adindowu.

“Mundivomereza kuti kulibe komwe munthu adayamba walembedwa ntchito mkumafuna angogikira kukwezedwa (promotion), mayenera kudutsa mu ndondomeko za milingo yosiyanasiyana. Mwa ichi tili ndi maudindo kufikira pansi penipeni, ndipo omwe akubwera kumene atha kukafikira mmaudindo amenewo koma osati ku likulu la chipani (NEC).

Ife monga komiti yoyendetsa chisankho tipanga zokhazo zomwe komiti yayikulu ya chipani (NEC) yatilamulira kuti tichite, ndipo sitichita chilichonse chosemphana ndi ziganizo za NEC. Ngakhale magomu omwe azitwngedwa kuyambira lolembali akuneneratu kuti ofuna kukapikisana nawo akhale amene wakwanitsa zaka ziwiri akutumikira chipani pa udindo wina uliwonse.” Anatero a Msukwa potsindika kuti amene sakufikira mulingo wa zaka ziwiri sakayima kuchisankhochi.

Mwa zina, chipani cha Kongelesi chakhazikitsa dipo lomwe ofuna kupikisana akuyenera kupereka. Mwa chitsanzo ofuna u Pulezidenti akuyenera kupereka K5,000,000, pomwe ofuna kukhala Wachiwiri kwa Mtsogoleri mchipanichi akuyenera kupereka ndalama yokwana K2,500,000.

Pakadali pano, palibe amene wabwera poyera kuti akufuna kukapikisana ndi Pulezidenti wa chipanichi, a Lazarus Chakwera kunsonkhanowu

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *