Pulezidenti Chakwera wati ulendo wa ku China upindulira Malawi

Kondanani Chilimunthaka

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati ulendo omwe anyamuka kupita mdziko la China ndi ofunika kwambiri chifukwa upindulira dziko la Malawi.

A Chakwera ati mkoyenera Malawi monganso maiko ena a muno mu afilika kukakhala nawo pa mkumano wapakati pa dziko la China lomwe pakadali pano lili pa nambala yachiwiri pa mndandanda wa maiko olemera kwambiri dziko lonse lapansi pofuna kuti zitukuko zosiyanasiyana mdziko muno zithe kupita patsogolo.

Polankhula pa bwalo la ndege la Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe lamulungu pa Sepitembala 1 pomwe amanyamuka kupita ku Beijing mdziko la China, Pulezidenti Chakwera anatsindika kuti ubale wadziko la Malawi ndi China ndiwofunikira kwambiri ndipo kuti ali mchikhulupiliro kuti ulendowu ukabala zipatso zokomera a Malawi.

“Mukudziwa kale kuti boma la China likudzipereka kuthandiza kukwanilitsa mfundo zathu za chitukuko, ndipo zomwe zachitikapo kale ndi chizindikiro kuti tikupita chitsogolo, ndipo gawo la chitukuko cha zomangamanga ndi limodzi la magawo omwe kupita chitsogolo tiyembekezere kuchokera kuboma la China” Anatero Pulezidenti Chakwera asadakwere ndege kupita mdziko la China.

Mkumanowu omwe ukungodziwika kuti FOCAC mwachidule ukuwunika za mgwirizano pakati pa dziko la China ndi mayiko a mu Afilika ndipo ukakhazikika poyang’ana ndondomeko zomwe zitsatidwe mzaka zitatu zikubwerazi pothandiza zitukuko zosiyanasiyana mmaiko a mu Afilika.

Pa ulendowu, Mtsogoleri wa dziko lino akuyembekezekanso kukakumana mwapadera ndi Mtsogoleri wa dziko la China komwe akuyembekezeka kukakambirana nkhani zolimbikitsa ubale pakati pa maiko awiriwa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *