Chakwera wati masomphenya a mipingo ndi boma ndi amodzi

Kondanani Chilimunthaka

Mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera komanso Mai wa fuko, a Monica Chakwera lero lamulungu pa 15 Disembala, 2024 anali nawo pa mwambo wa mapemphero pa mpingo wa Katoto Assemblies of God mu mzinda wa Mzuzu.

Polankhula, Mtsogoleri wa dziko linoyu analimbikitsa mpingowu kuti upitilire kulalikira za kutembenuka mtima zomwe zikufanana ndi mfundo ya boma yosintha kaganizidwe pofuna kupereka chiyembekezo chotukulira dziko lino komanso kuti anthu alape machimo.

“Tilape, tidzikhuthule pa maso pa Yehova, kuti Mulungu atimvere chisoni, atithandize popeza amatikonda, ndipo safuna wina akhale kunja. Kotero tiphunzire kuti palibe mmodzi amene ali osafunika pamaso pa Mulungu” Anatero Mtsogoleri wa dziko lino.

Polankhula poyambilira, m’busa *Raphael Ndewere* wa mpingo wa Katoto Assemblies of God anati mpingowu ndi okondwa kuti mtsogoleri wa dziko lino ndi Mai wafuko, anasankha kukapemphera nawo pa mpingowu, ponena kuti dzina la Pulezidenti Chakwera lili mumbiri pokhala m’busa amene anakhazikitsa maziko a mpingo wa Katoto Assemblies of God, zaka zambiri zapitazo.

Koma m’busa Raphael Ndewere anaonjezera mkuthokoza Mtsogoleri wa dziko lino ponena kuti pokhala mpingo, ukamaona azimayi akupatsidwa maudindo akuluakulu umalimbikitsika kuti utsogoleri wa Pulezidenti Chakwera ukulemekeza azimayi mdziko muno.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *