Mtsogoleri wa dziko lino wakhazikitsa ntchito ya ndondomeko ya AIP ya 2024/25

Kondanani Chilimunthaka

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Lazarus Chakwera lolemba pa Okotobala 14, 2024 anali m’boma la Neno kukakhazikitsa ntchito ya mundondomeko yagulitsa zipangizo za ulimi zotsika mtengo za mchaka cha 2024/2025 pa mwambo omwe unachitikira pa sukulu ya Pulayimale ya Dzundu kwa mfumu yayikulu Symon m’boma la Neno.

Polankhula kukhwimbi ya anthu pomwe amakhazikitsa ntchitoyi, Mtsogoleri wa dziko lino anati akudziwa kuti mdziko muno mwagwa njala yayikulu, popeza konse komwe akuyenda a Malawi akudandaula za vuto la chakudya. Koma iye anati a Malawi akudziwanso bwino kuti njalayi yabwera kamba ka mavuto a kusintha kwa nyengo.

Chakwera anati alimi mdziko muno sanganamizidwe kuti njala abweretsa ndi iye, popeza akudziwa bwino vuto la nyengo lomwe amakumana nalo mminda yawo mchaka chapitachi.

“Mlimi tikamupatsa fetereza ndi zipangizo za ulimi motchipa amadziwa kuti amene tamuthandiza kupeza chakudya ndifeyo. Ndipo chimanga chiakonongeka asadakolore amadziwa kuti amene timufikire ndi chakudya chogawa ndifeyo, osati aja amangokhalira kunama bodza kuti boma ndilimene labweretsa njala.

Ndiye lero ndabwera kuno ku Neno kudzakhazikitsa pologalamu ya AIP kuti alimi nonse amene muli ndi kuthekera kolima chakudya mupezeko fetereza otchipa” Anatero Mtsogoleri wa dziko lino.

Pulezidenti Chakwera anatsindika kuti ndondomeko ya AIP ndi ya a Malawi okhawo omwe ali ndi kuthekera kolima chakudya osati aliyense ngakhale amene alibe munda, ponene kuti omwe sakukwanira kupindula mundondomeko ya AIP, kapena sali pa mndandanda opindula nawo mundondomekoyi, athandizidwa kudzera mundondomeko zina za boma lake monga Mtukula pakhomo, komanso ngongole kudzera mu bungwe la NEEF.

Chaka chino alimi oposa 1 miliyoni ndamene akuyembekezeka kupindula fetereza, komanso mbeu ndi ziweto mundondomeko ya zipangizo zotsika mtengo ya AIP.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *