Nduna yoona za ma boma ang’ono a Richard Chimwendo Banda apempha mafumu kuti athandize mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera pa nkhondo yake yolimbana ndi ziphuphu ndi katangale.

Polankhula pamwambo okweza ma ufumu awiri kukhala mafumu andodo (Traditional Authorities) ku Mchinji , a Chimwendo anati mafumu ndi ofunika kwambiri pa ntchito yokweza dziko lino.

Mwaichi a Chimwendo anapempha mafumu okwezedwawo kuti agwire ntchito ndi boma apewe umuthira kuwiri ndipo athandize mtsogoleri wadziko lino pomenyana ndi katangale. Iwo anati , Katangale ndi mdani wamkulu wadziko lino.

Mmawu ake mfumu yaikulu Mavwere idayamika boma kamba ka ganizo lake lokweza mafumu awiriwa omwe ndi a Ndawambe ndi Pinda.

A Mavwere adati mafumu awiriwa agwira ntchito yaikulu maka pa nkhani zachitukuko mboma la Mchinji.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *