Kudali munthu wa mundipondera mwana lero pa bwalo la zamasewera la Chigodi pamene phungu wa delaro a Simplex Chithyola Banda yemwenso ndi nduna ya zachuma anali ndi msonkhano.

A Banda anapha mbalame ziwiri ndi mwala umodzi chifukwa iwo kupatula kukawayankhula wanthu pankhani ya dziko, anakacheza nawo wanthu monga tsiku lawo lobadwa.

Mmawu awo a Chithyola adauza wanthu kuti asadandaule chifukwa mabvuto adzachuma omwe dziko lino limakumana nawo akhala mbiri yakale.

Iwo anati boma lakonza njira zambiri zomwe zithandize kukonzanso chuma cha dziko lino.

A Chithyola anauzanso anthu pa msonkhano kuti asadandaule chifukwa pompano boma liyamba kugawa chimanga chaulere matumba awiri pa banja lililonse.

Kumsonkhanoko kunabwera aphungu pafupifupi makumi awiri (20) ndi nduna zisanu.

Zina mwa nduna zinabwela kumsonkhano ndi monga nduna ya za migodi, a Monica Chang’anamuno, Nduna ya umoyo a Khumbize Kandodo Chiponda, Nduna ya zamalo Deus Gumba, ndinso Nduna ya za maboma ang’ono a Richard Chimwendo Banda.

 

 

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *