Malawi Exclusive 

Mlembi wamkulu wa chipani cha Kongeresi, Richard Chimwendo walimbikitsa otsatila chipanichi kuti agwire ntchito molimbika popititsa chipani patsogolo monga momwe chimachitila tcheni cha njinga pa kalanka.

A Chimwendo ayankhula izi Lolemba ku Chileka mu mzinda wa Blantyre komwe chinamtindi cha otsatila chipanichi chinasonkhana pofuna kuti mtsogoleri wawo Dr. Lazarus McCarthy Chakwera awayankhule asanabwelere ku Lilongwe.

Iwo anati nthawi yoti otsatila chipani chachikulu cha MCP awonetse kusagwededzeka kapena m’mbuyo ndi ino pamene chipanichi chiri kunja kwa boma.

“Khalani anthu osagwedezeka ndi mphepo komanso olimba pa ulendo wokwera mtunda momwe chimachitira tcheni pa cha njinga pa kalanka,” anatsindika motero a Chimwendo.

Pamfundoyi, mlembi wamkuluyu anadzudzula anthu omwe awonetsa kusalimba mtima mkatikati mwa chaka chimodzi kuchokera pa 16 September chaka chatha pomwe chipani cha MCP chidaturuka m’boma.

Akulu-akulu ochuruka kuphatikidzapo mneneri wa chipanichi, Dr Jessy Kabwira anali nawo pa nkhumanowu atavala nkhope za chimwemwe pokhala ndi mpata wonga uwu wocheza ndi mtsogoleri wawo.

#MalawiExclusiveOnline

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *