Tate wadziko lino Dr Lazarus Chakwera lero adali pamwambo otsekulira sukulu ya Malawi School of Government ku Kanengo mumzinda wa Lilongwe. Mmawu ake Chakwera wachenjeza mchitidwe wa ulesi komanso onyozera mwadaladala malamulo pakati pa anthu ogwira ntchito m’thambi zonse za boma. Pofuna kuti mchitidwewu uthe munthambi zonse zaboma Dr Lazarus chakwera walamula m’lembi wamkulu mu office ya mtsogoleri ndi nduna mayi Collen Zamba kuti awonetsetse kuti akulu akulu a maudindo munthambi za boma apita ku sukuluyi kuti pakhale kusintha pakagwilidwe ka ntchito m’nthambi zonse. Mtsogoleri wa dziko linoyu anamaliza ndikunena kuti nthawi yomwe amalowa mboma anapeza kuti akulu akulu mnthambi zaboma ankagwira ntchito zawo kwambiri mosatsatira malamulo koma kubwera kwa sukuluyi kuthandiza kupitsa ukatswiri pakagwilidwe ka ntchito boma. Post navigation Chakwera describes tobacco industry as country’s major forex earner Chakwera ayamikira sukulu ya Malawi Government kuti ithandiza kukweza ntchito za boma