Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwer watsekulira ntchito za sukulu ija poyamba imatchedwa Malawi Institute of Management (MIM) ndipo pano idzitchedwa Malawi School of Government (MSG).

Mukulankhula kwawo, a Chakwera awuza a Malawi za kufunika kwa sukulu za mtundu umenewu.

“Ndiye sukulu imeneyi ndi njira imodzi yoonetsetsa kuti zifukwa zonse zopangitsa anthu am’boma kuti azigwira ntchito monyinyirika tithane nazo, chifukwa amene akumasafala ndi mchitidwe waulesi ndi onyinyirika pantchito ndi a Malawi. Ndichifukwanso ine ndiri okondwa
kuti tikukhazikitsa Individual Performance Management System m’bomamu, mogwirizana ndi a Chandler Institute of Governance, ndi cholinga choti tonse ife ogwira ntchito m’boma tiziunikirana mmene tikuwatumikila a Malawi,
chifukwa amene akunyinyirika pa ntchito yowatumikila a Malawi, sibwino kuti tizimusekelera. Mr. Richard Chandler
amene anayambitsa Chandler Institute of Governance,” Adatero a Chakwera.

Chakwera adapempha ogwira ntchito mboma kuti akamapanga ziganizo azipnga ziganizo zakupsa komanso zopindulira a Malawi.

Achakwera adati nzomvetsa chisoni kuti pali anthu wena amene amagwira ntchito mosalumikizana ndi maofesi ena aboma zomwe adati nkulakwa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *