Kondanani Chilimunthaka Mtsogoleri wa dziko lino, a Lazarus Chakwera ayamikira alimi a mbeu ya fodya mdziko muno poyika chidwi kusamalira fodya wawo, ponena kuti izi zapangitsa kuti mitengo ya mbeuyi ikwere pa msika. Mtsogoleri wa dziko linoyu amalankhula izi potsekulira chiwonetsero cha malonda mu mzinda wazalonda wa Blantyre chomwe mcha nambala 34. Malingana ndi Pulezidenti Chakwera, alimi a fodya ndi okondwa ndi mitengo yomwe akupatsidwa kumisika yonse mdziko muno chifukwa boma lawo lawamenyera nkhondo yogulitsa fodya wawo pa mitengo yabwino kuposa kale. “Wina asakunamizeni kuti ulimi sukuyenda ku Malawi kuno chifukwa ngakhale m’misika ya fodya mdziko muno, kaya ndi ku Mzuzu, kaya ndi ku Kasungu, ku Lilongwe komanso kuno ku Limbe, mukapeza kuti alimi a fodya ali ku Kenani chaka chino” anatero Mtsogoleri wa dziko lino powonetsa kukondwa kwake ndi momwe alimi akupindulira ndi mbeu ya fodya pa msika ovomerezeka. A Chakwera anathokoza makampani ogula fodya, ponena kuti mitengo yomwe akupereka ilimbikitsa bizinesi ya ulimi kuti ipitilire kukhala yotentha mdziko la Malawi. Iwo anathokonzaso alimi pogwira ntchito molimbika, kutsatira uphungu wa malimidwe a makono, komanso pochepetsa za chinyengo zomwe Pulezidentiyu anati zapangitsa kuti ogula mbeuyi azikhutira. Komabe Mtsogoleri wa dziko linoyu anati chatsalira tsopano ndi chakuti zomwe zikuchitika ku bizinesi ya fodya zichitikenso ku bizinesi ya mbeu zina, ndipo anati boma lake likufuna kuthandiza alimi a mdziko muno mwakathithi. Koma a Chakwera anatsindika kuti mpofunika boma ndi amalonda omwe sali mkhwapa mwa boma agwirane manja kuti ndondomeko zonse zifikire posintha chuma cha dziko lino, ponena kuti Boma ndilokonzeka kupatsa a malonda mwai ogulitsa katundu wawo kunja kwa Malawi kudzera mundondomeko mzosiyanasiyana kuphatikizapo zokopa alendo ndi za migodi. Polankhula poyambirira, nduna yowona za Malonda ndi Mafakitale, a Sosten Gwengwe anayamikira Pulezidenti Chakwera ndi boma lake kamba kowonetsa chidwi pa ntchito za malonda mdziko muno, komanso kupereka danga kwa amalonda osiyanasiyana lokweza nawo ntchito za malonda potukula chuma cha dziko la Malawi. Chionetserochi chomwe chayamba lachinayi pa 23 Meyi chidzatha lachitatu pa 29 Meyi chaka chino. Post navigation NBM Plc bankrolls Beerland Festival with K15 million FDH Bank plc commits to sustaining profits