Mzimayi yemwe dzina lake ndi Alinafe Chidwala wapepesa ndikuchotsa makanema omwe anayika pamasamba amchezo onena kuti nduna yazachitetezo chamdziko Ken Zikhale Ng’oma adakamusumira pankhani yamalo zomwe azikhale Ng’oma anati kunali kungofuna kuwawonongera mbili chabe.

Malingana ndi uthenga omwe a Chidwala alemba patsamba lawo la Facebook kumadzulo no, Iwo akupepesa Kwa a Zikhale Ng’oma ndipo kuti analibe malingaliro aliwonse olakwika poyika makanemawa.

Kudzera mwa oyimira anthu pa milandu Oscar Tauro yemwenso watsimikiza zankhaniyi, Ndunayi inawuza mzimayiyu kuti achotse mmasamba amchezo kanemayo ndikupepesa pasanadutse maola 24 apo bi, ndunayi ikamang’ala kuti Chidwala apeleke 200million kwacha powaonongela mbili.

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *