Malingana ndi chikalata chomwe unduna owona zachitetezo cha mdziko , mtsogoleri wadziko lino wakhululukira akaidi okwana 35.

Izi zachitika ngati njira imodzi yosangalarira ufulu omwe dziko la Malawi likudyerera pansi pa ulamuliro wa Dr Lazarus McCarthy Chakwera ndi chipani cha Malawi CongressParty(MCP) .

Malingana ndi chikalata chimenechi Mtsogloeri wadziko amapatsidwa mphamvu kuchokera ku gawo 89 la malamulo adziko lino.

Anthuwa ndi omwe agwira theka la chigamulo chawo chomwe bwalo lidawagamula kuti agwire.

Komanso wena omwe adali odwalika kwambiri , okalamba komanso azimai omwe adapalamula ali ndi ana.

Malingana ndi chikalata , Chakwera wachepetsanso zilango ndi minyezi isanu ndi inayi 9 kwa aliyese opalamula ngati njira imodzi yochepetsera kuthithikana.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *