A Malawi ambiri m’mzinda wa Lilongwe ayamikira mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus McCarthy Chakwera kamba koyambitsa ntchito yomanga likulu la mabwalo amilandu mdziko muno. Malingana ndi a Malawi omwe adayankhula ndi atolankhani anthu, ntchito iyi ipereka mwayi kwa a nzinka zambiri zokhala mumzindawu kuti zipeze mwayi wa ntchito. Malingana ndi nzikazi, wenanso ambiri omwe amapanga ntchito za malonda akhalanso ndi mwayi opanga ntchito zawozo. Iwo adapereza chitsanzo cha anthu omwe amapanga malonda azipangizo zomanga manga kuti adzakhala ndi mwayi operekera katundu wawo kuntchito yomanga likulu la mabwalo a zamilandu. Ndondomeko zomanga ntchito iyi pakadali pano zikuyenda bwino. Boma lapereka kale ndalama zokwana K600Million zomwe zagwira ntchito zosiyana siyana zokhudza kuyamba ku ntchito imeneyo. “Ine ndi Aisha Banda ndimakhala kwa Kauma. Ndati ndinene kuti ndine okondwa kwambiri kuti ntchito pano ikuyambika. Ndithokoze abwana a Chakwera kamba koikapo mtima kuti izi zitheke tikudzikuwa ena aja ankangonena koma awa akwanitsa,” Kudzera ku ntchito imeneyi, boma limanga likulu la Bwalo lalikulu la ,(high Court) komanso bwalo la supreme , ndinso pazakhalanso ma likulu onse a mabwalo a milandu. Ntchito ithandiza kupititsa patsogolo mwayi oti anthu azipeza chilungamo mosavuta pansi pa boma la Dr Lazarus Chakwera. Post navigation Chakwera akhululukira akaidi okwana 35 munyengo yokumbukira zaka 60 Malawi ali pa ufulu odzilamulira Kupha makwacha munthawi ya Chakwera; Malawi wapeza ndalama zokwana $353.9mn kuchokera ku ulimi wa fodya