Dziko la Malawi pansi pa utsogoleri wa Dr Lazarus McCarthy Chakwera ndi lodala maka pa nkhani ya ulimi wa fodya.

Malawi tikunena pano wapeza ndalama zokwana $353.9Million pa masabata khumi ndi awiri (12).

Malingana ndi ma report omwe bungwe bungwe la AHL limatulutsa , mtengo wafodya wakhala ukukwera.

Malingana ndi malipoti amenewa fodya wakhala akugulitsidwa pa mtengo wa $2.94 omwe wakwera ndi mlongon wa 27 % tikafananiza ndi wa chaka chatha omwe unali $2.33 panthawi monga iyi.

Tikunena pano fodya okwana 103.2 million kilograms ndi yemwe wagulitsidwa.

Malingana ndi mneneli wa bungwe loona za fodya la Tobacco Commission, Fodya wakhala akugulitsidwa pa mtengo wa $3.59 zomwe akuti sizinachitikepo m’mbiri wa malonda a fodya.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *