Nduna ya zamdziko a Dr Ken Zikhale Ng’oma ayamikira tate wadziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera kamba kokhala mtsogoleri oyamba yemwe wakwanitsa kusintha Malawi pakanthawi kochepa.
Mukulankhula kwawo ku Karonga pomwe iwo adakumana ndi anthu omwe amavota ku msonkhano waukulu wa chipanichi omwe uliko pa 8 ndi 9 August,  a Ng’oma ati pakufunika anthu amphamvu odziwa ntchito kuti athandize a Chakwera apambane masankho omwe akubwera mu 2024.
Iwo ati ndidzachidziwikire kuti masankho akubwerawa ndi ofunikira kwambiri choncho pakufunika akatswiri amphamvu omwe akudziwa ntchitoyi kuti amthandize Chakwera.
A Zikhale adati, iwo agwira ntchito yaikulu kuika atsogoleri mu mipando choncho nthawi yakwana kuti ndithandizenso a Chakwera kuti alowenso mboma.
Iwo adati osewera bwino mpira ngati Ronaldo samuika pa benchi.
Mukulankhula kwawo nduna ya masewero a Uchizi Mkandawire,  adauza wanthu kuti akavotere a Ng’oma ngati wachiwiri oyamba kwamtsogoleri wa chipani cha MCP chifukwa ndi munthu okonda Chipani komanso anthu otsatira chipanichi.
A Mkandawire adati a Dr Zikhale Ng’oma ndi munthu yekhayo yemwe angakwanitse kuthandiza a MCP kuti isatuluke mboma.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *