Mchaka cha 2013 maiko ndi bungwe onse amene amathandiza dziko lino adalengeza kuti asiya kuthandiza dziko lino kamba ka ziphuphu ndi katangale zomwe zinkachitika nthawi imeneyo. Atangolowa mboma , onse anabwerelera nkuyambanso kuthandiza dziko lino. Ichi nchifukwa chake Nduna yazachuma a Simplex Chithyola Banda yati anthu oposa 570,000 omwe adakhudzika ndi mavuto akusintha kwa nyengo apindula ndi ndalama pafupifupi K94 billion zochokera ku thumba la Green Climate Fund (GCF). A Chithyola adanena izi pomwe amasainilana mgwirizano ndi bungwe la Food and Agriculture Organisation (FAO) pa mwambo omwe unachitikira ku unduna wazachuma. Iwo ati mavutowa adza mdziko lino kamba ka anamondwe, ng’amba komanso kusefukira kwa madzi mwa zina. Thandizoli ladza pasanathe mwezi a Chithyola limodzi ndi akulu akulu ena a boma atachita zokambirana ndi akulu akulu a GCF ku South Korea. Pakali pano ndunayi yati thandizoli ladza kutsatira chikhulupiliro chomwe maiko ndimabungwe ali nacho muutsogoleri wa president Lazarus Chakwera, ndipo alonjeza kuti ndalamazi zigwira ntchito yoyenera posintha miyoyo ya anthu ovutika. Mmau ake nthumwi ya bungwe la FAO mdziko lino a Zihjun Chen wayamikira dziko la Malawi ndi bungwe la GCF chifukwa chowakhulupilira kuti atsogolele pa ntchitoyi. Ntchitoyi igwirika mmaboma osankhika khumi ndi limodzi mdziko lino. Post navigation Ukhondo ndi ofunika: Sagawa atsogolera ntchito yosesa mumzinda wa Lilongwe Chakwera hits the ground running meets UAE Govt officials