Atagwira ntchito monga yomweyi sabata yatha, Mfumu yaikulu ya mzinda wa Lilongwe a Esther Sagawa, lero inatsogoleranso ntchito yosesa mumzinda wa Lilongwe.

Mukulankhula kwawo a Sagawa anati iwo adalonjeza kubwezeretsa ukhondo mumzinda wa Lilongwe ndipo izi akuti zipitilira ndi cholinga choti ukhondo ubwere.

A Sagawa anenetsa kuti mzinda wa Lilongwe udali wa ukhondo kale ndipo anati umatchuka kwambiri kamba ka ukhondo umenewu.

Iwo apempha nzika zokhala mumzindawu kuti zisamataye zinyalala paliponse kuti mzindawu uzioneka bwino.

Mukulankhula kwawo mmodzi mwa anthu omwe amasesa nawo, a Robert Banda anayamika a Sagawa kamba koika mtima pankhani yokonzanso mzinda wa Lilongwe.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *