A MKAKA KUYANKHULA NDI ATOLANKHANI Mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) a Eisenhower Mkaka wapempha adindo ndi onse okhudzidwa kuti alangize a Malawi kuti apewe mchitidwe ogulitsa zipangizo za ulimi zotsika mtengo za mu ndondomeko ya AIP. HON. BABA MALONDELA BRIEFING JOURNALISTS A Mkaka anena izi lamulungu pa bwalo la zamasewero la Danda mmudzi wa mfumu yaikulu Kalumbu mboma la Lilongwe pamene iwo anali mlendo olemekezeka pa mwambo opereka mphoto kwa opambana ku mpikisano wa zamasewero a Baba Malondera K5 million Football Trophy. Mmau ake Mkaka anati boma limaika ndalama zambiri ku ndondomeko ya imeneyi choncho nkulakwa kuti anthu ena azigulitsa zipangizozi. Ndipo mmawu ake Malondera anayamika boma motsogozedwa ndi President Dr Lazarus McCarthy Chakwera kamba ka zitukuko zosiyanasiyana zomwe zachitika pansi pa utsogoleri wa Malawi Congress Party (MCP). Malondera wati anthu m’dela lake akumwa madzi a mmipopi komanso kwamangidwa sukulu zambiri kudzanso milatho ndi zipatala. Iye anati izi zachitika kamba ka utsogoleri wa Chakwera omwe udakweza ndalama ya CDF kuchokera pa K30 million kufika pa K100 million. Post navigation Chilumba depot AIP officials accused of extortion President Chakwera praised for Mega farm initiative