Mtsogoleri wadziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera waonetsa chamuna podzutsa Sukulu ya ukachenjede ya pamwamba ku mpoto mboma la Mzimba. Sukulu iyi ndi imene inkatchedwa Mombera kale koma boma ili la Chakwera lasintha dzina pano ndi Inkosi ya Makhosi Mbelwa. Zomwe akupanga Chakwera ku Mzimba zakondweretsa aliyese kumeneku. Chifukwa a Malawi kumeneku akhala ndi mwai opeza ntchito. Benjamin Chirwa wamudzi mwa Chigwa omwe wazungulira sukulu ya Inkosi ya Makhosi Mbelwa wati ndi okondwa chifukwa dela lakwawo lipindula kwambiri kamba ka izi. Naye Bwana mkubwa wa Mzimba a Rodney Simwaka ati ndi okondwa kwambiri kamba ka izi. Sukulu imeneyi idya ndalama zokwana K450Billion. Post navigation Zikhale engages chiefs on developmental projects Inkosi ya Makhosi M’mbelwa urges communities surrounding M’mbelwa University to support the project