Mzinda wa Blantyre unagwedezeka kuti gwede lero pamene mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera amalowa mu mzindawu pa ulendo wawo ochokera ku Lilongwe.

A Chakwera afika lero mu Blantyre kudzela ku bwalo lija la ndege la Chileka.

M’mawu ake wapampando wa chipani cha Malawi Congress a Peter Simbi anayamikila a Chakwera kamba ka ulendowu.

A Simbi anati bwanawa azibwerabwera ku ku mmzindawu kuti azitha kumazionela okha mavuto ena amene anthu amakumana nawo pa umoyo wawo watsiku ndi tsiku.

Naye mkulu okopa anthu m’chipanichi a Moses Kunkuyu anayamika a Chakwera kamba ka ulendo umenewu.
Achakwera akhala kummwera kuti agwire ntchito zingapo muchigawochi.
Mwazina iwo akakhala mlendo olemekezeka pa mwambo okumbukila malemu Mbusa John Chilembwe.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *