Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus McCarthy Chakwera apempha a Malawi mdziko muno kuti apewe mkhalidwe odzikonda podziunjikila ndalama kudzera mnjira yakuba ndi katangale. A Chakwera amayankhula izi pamsomkhano wa chitukuko omwe anachititsa pa sukulu ya Katerele uku ndi Salima. A Chakwera analimbikitsa ogwira ntchito mboma kuti akuyenera kugwiritsa ntchito bwino ndalama zaboma zomwe ndi za a Malawi. DR LAZARUS CHAKWERA Pamsonkhano umenewo a Chakwera analandila a Uladi Mussa omwe alowa mchipani cha Malawi Congress (MCP). Post navigation MCP takes the Gospel of Building a new Malawi to Area 25 this weekend Katswiri pankhani za ndale adzudzula DPP kamba kodelera ziganizo za ma bwalo a milandu