Katswiri odziwika bwino pankhani za ndale komanso omwe amayankhulapo pam’mene zinthu zikuyendera mdziko muno a Ceazer Kondowe adzudzula utsogoleri wa Chipani cha Democratic Progressive (DPP) kamba kosowa mwambo komanso kamba kolephera kutsatira chiganizo cha bwalo la milandu.

M’mwezi wa August 2022, a Kondwani Nankhumwa adakatenga chiletso choletsa a George Chaponda kuti asakhale mtsogoleri wa otsutsa mnyumba ya Malamulo.

MR CEASER KONDOWE

Anankhumwa anakatenga chiletso ichi chipani cha DPP chitalengeza kuti chasintha utsogoleri wa mnyumbayi.
Mukulankhula kwawo a Kondowe ati ndizomvetsa chisoni kuti Chipani cha DPP chikupitilizabe mkhalidwe wake ophwanya malamulo.

Iwo adati Nankhumwa pakadali pano sangasinthidwe kukhala munthu wamba kapena kuti sangachotsedwe mphamvu za udindo wawo chifukwa pali chiletso chomwe iwo adakatenga ku bwalo la milandu.

Malingana ndi a Kondowe, DPP isamataye nthawi kuloza dzala anthu osalakwa monga a Gotani Hara pamene bvuto ndi utsogoleri ku chipaniku omwe sufuna kumvera ziganizo za mabwalo a milandu.

Iwo anapitiliza kuchenjeza cha DPP kuti chidekhe ndipo alore ma lamulo agwire ntchito yake.

“DPP ikuyenela kudziwa kuti kulakwa kutengera malamulo m’manja liyese akudziwa kuti ndi mlandu kuphwanya ziganizo za bwalo, ” Adatero a Kondowe.

Iwo adati palibe nkhani ya chilendo apapa chomwe DPP ingapange ingopita ku bwalo la Milandu ikachotse chiletso chomwe a anatenga a Nankhumwa basi mmalo moloza utsogoleri wa nyumba ya Malamulo.

“Pitani kachotseni chiletso chomwe a Nankhumwa adatenga ndipo tinene mobwereza pitani ku Khoti zonse mukathane nazo mmalo momangonyoza, ” Atero a Kondowe.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *