Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus McCarthy Chakwera pofuna kuonetsetsa ndi munthu ofunika zabwino a Malawi , wakana pempho lomwe zipani zotsutsa zidabwera lofuna kuti boma lizipereka chuma choyendetsera zipanizo.

Malingana ndi chikalata chomwe mnebeli wa kunyumba ya boma watulutsa a Anthony Kasunda, pempho limeneli likutsutsana ndai gawo 40 lamalamulo a adziko akulu adziko lino.

Phungu wa DPP ku Mulanje Bale, a Victor Musowa adabweretsa ku nyumba ya malamulo bill yofuna kuti DPP ndi zipani zina zotsutsa boma zizilandira ndalama ku boma zochitira ntchito zawo za tsiku ndi tsiku.

Koma mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus McCarthy Chakwera safuna kuti zipani za ndale ziwononge chuma cha boma ndipo sadavomereze kuti zikhazikike ngati lamulo.

Apa zikutanthauza kuti zipani zonse zipitiliza kudzipezera ndalama zogwiritsa ntchito kamba koti DPP kuzolowera kwake kusakaza ndalama za boma.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *