Nduna ya zamtengatenga m’dziko muno a Jacob Hara ati boma la Malawi pansi pa utsogoleri wa Dr Lazarus chakwera pakali pano wapeza ndalama zomwe zithandize kukonzaso miseu yomwe idaonongeka chifukwa cha kusefukira kwa madzi ndi Namomdwe wa Freddy.

A Jacob Hara alankhula izi lero ku nyumba ya malamulo poyankhapo mafuso omwe aphungu nyumbayi anafusa kuti afotokoze pa zomwe unduna wawo ukuchita pa nkhani yokozaso miseu-yi.

A JCOB HARA – NDUNA YA MTENGATENGA

A Jacob Hara anamaliza ndikunena kuti ntchitoyi yachedwelapo chifukwa yakumana ndi mavuto akutsika kwa ndalama ya dziko lino,koma pakali pano zonse zili mchimake.

Mvula yambiri ya Mphepo yamkuntho mu chaka cha 2023 idaononga katundu wambiri komanso miyoyo yochuluka.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *