Pomwe mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus chakwera akupitiliza kukwanilitsa malonjezano ake, la chitatu pa 21 February 2024 , 2 koloko masana , akuyembekezeka kukaonekera ku nyumba ya malamulo komwe akukayankha mafuso kuchokera kwa aphungu m’nyumbayi. Chitengeleni boma m’chaka cha 2020 Dr Lazarus chakwera wakhala akufika ku nyumbayi kukayankha mafuso pokwanilitsa lonjezo lake kuti ndikadzalowa boma ndizizapita ku nyumba ya malamulo kukayankha mafunso a momwe dziko lino likuyendera. President Dr Lazarus McCarthy Chakwera Mwachitsanzo mu March 2023, Chakwera adadabwitsa anthu mmene iye adayankhira mafunso munyumbayi. Chakwera wakhala akukayankha mafunso nthawi yonseyi chitengereni boma. Post navigation Malawi participates in R & A Africa Amateur Golf Championship in SA NCHE hails NBS Bank partnership on digital payments